Skip to Content (Press Enter)

One for All (Chichewa)

  • Posted by Bella,
  • Director,
  • in Listen up,
  • November '22

Tsatirani Tadala ndi Mayeso powerenga kabukuka pomwe ali nkati mofuna kupeza mayankho amafunso awa: Kodi timvere ziti, nanga tikhulupirire ndani pa nkhani za katemera?

Kabuku ka One for All, All for One ka ndi kaulele, ndipo cholinga chake ndi kuthandiza anthu kuti azikambirana mwa makono za katemera, chitetezo cha gulu, chikhulupiriro pa katemera komanso kugwira ntchito ya kafukufuku limodzi.

Padziko lonse lapansi anthu omwe ali pa chiopsezo cha matenda opatsirana ndi amene amakhala pa mavuto akulu pomwe ntchito za katemera zasokonekera. China chomwe chimasokoneza ntchito za katemera kwambiri ndi kusowa kwa katemera. Ngakhale izi ziri chonchi, njira zomwe timagwiritsa ntchito pofalitsa mauthenga a katemera komanso kukhala ndi chikhulupiriro pa katemera ndi zinanso zofunika kuziganizira kwambiri.

Katemera samangothandiza munthu amene walandilayo ayi komanso amathandiza anthu omwe ayandikana nawo, ichi ndi chifukwa chomwe kafukufuku wa katemera amapangidwa pogwirira ntchito limodzi ndi anthu osiyana siyana monga odwala komanso anthu ochokera m’zigawo zosiyana siyana.

Pulojekiti ya One for All, All for One ndi pulojekiti yomwe yagwira ntchito ndi anthu osiyana siyana, ochokera m’maiko monga Malawi, South Africa ndi UK. Kudzera mu m’gwirizano umenewu takhazikitsa njira za makono zothandizira anthu kukambirana za katemera komanso m’mene anthu angagwirire ntchito yakafukufuku limodzi – Kabuku ka One for All, All for One.

Zinthunzi za kabukuka zinajambulidwa ndi MO, yemwe kwawo ndi ku South Africa, ndipo nkhani yake ikukamba za Tadala ndi Mayeso, omwe azunguliridwa ndi chimpwirikiti cha zokamba kamba za anthu, ndipo iwowa akufunitsitsa ataunikira bwino bwino zakambidwazi kuti apange ziganizo zawo paokha zokhudza katemera. Ndi thandizo lochokera kwa makolo awo, a za sayansi komanso anthu aku dela lawo azindikira njira zomwe angagwiritse kuti athe kutenga nawo gawo mu kafukufuku.

Cartoon of three people embracing in a hug

Kabukuka kakusonyeza nzeru zomwe a chinyamata , ana a sukulu, magulu akumudzi, makolo ochembeza kumene, alangizi a zaumoyo, atsogoleri a m’madela komanso m’mipingo, ojambula komanso a zakafukufuku a ku ulaya komanso ku Afilika kuno anaikapo pokonza kabukuka. Kupatula izi, kabukuka kanakonzedwanso molingana ndi zotsatira za kafukufuku yemwe anapangidwa kwa anthu osiyana siyana.

Mutha kupeza kabukuka m’musimu, ndipo kali mu Chingelezi komanso Chichewa! Ndipo tidzakhala okondwa kwambiri ngati mungawagawileko anthu ena omwe mulinawo pafupi angakhale omwe ali kutali nanu. Ngati mukufuna mabukuwa osindikizidwa kale oti mugawileko anthu m’dela lanu, lankhulani ndi ife kudzela pa vocal@mft.nhs.uk Tithanso kuthandizana nanu potanthauzira kabukuka komanso kanema kuti mugwiritse ntchito ku maiko ena.

Tili ndi chikhulupiriro kuti musangalala ndi khaniyi!